Chiyanjano is one of the tracks on Lucius Banda’s Down Babylon Album. Some of his songs were politically motivated but it is not clear what inspired him to write this one.
Chiyanjano is written from the point of view of a person who’s talking to his uncle. The uncle had a lot of power and abused it...
[Chorus]
Oooh chiyanjano, chiyanjano
Ndicha ntundu wanji?
Oooh chiyanjano, chiyanjano
Chinkandidabwitsa
[Verse 1]
Chiyanjano chanu chonde amalume
Ndi gulu lanu chinkandidabwitsa
Ufumu wanji wapa chiweniweni
Ndinkadziwa izi sizidzatha bwino
Ubwezi wanji wosa dzuzulana
Tikudana, tikutha anthu athu
Jakisoni ochiritsa anthu
Ndiyemweyo inu munkaphera anthu oh!
[Chorus X2]
[Verse 2]
Lero muku[?] taganizani ndalama ndi za chani izi?
Mano akatha musamaswe phale
Mulekere wana apitilize kukazinga
Chifundo chake chiribe malire
Mukumbukire mbala pa ntanda paja
Ndalama mwabisazi mukanapatsa amphawi
Mukanagula Ufumu wa Kumwamba oh!
[Chorus X2]
[Verse 3]
Malume zinthu zikamangoyenda bwino
Zikavuta, zikavuta zimavutiratu
Malume maudindo anachulukitsa
Ndinkadziwa mudzathera m'ndende
Azakhali nawo kuuma ntima
Munthu wa mayi koma m'maso muli gwa!
Ndalama mwabisazi mukanapatsa amphawi
Mukanagula Ufumu wa Kumwamba oh!
[Chorus X2]
[Chorus X4]
Lucius-banda released Chiyanjano on Wed Jan 01 1997.